Leviticus 5:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwa posapereka kwa Chauta zinthu zopatulika zofunika, koma mosadziŵa, apereke kwa Chauta nsembe yopepesera kupalamula chifukwa cha tchimo lakelo. Nsembe yake ikhale nkhosa yamphongo yopanda chilema, ndipo mtengo wake wa nkhosayo udzakhale wokwana masekeli asiliva, potsata kaŵerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera kupalamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akachita mosakhulupirika, nakachimwa osati dala, pa zopatulika za Yehova, azidza nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema, ya m'gulu lake, monga umayesa mtengo wake potchula masekeli a siliva, kunena sekeli wa malo opatulika, ikhale nsembe yopalamula;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwa mosadziwa posapereka zinthu zopatulika zofunika kwa Yehova, munthuyo apereke kwa Yehova nsembe yopepesera machimo ake. Nsembeyo ikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake ukhale wokwana masekeli oyenera a siliva pakawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu. Imeneyi ndi nsembe yopepesera kupalamula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akacita mosakhulupirika, nakacimwa osati dala, pa zopatulika za Yehova, azidza nayo nsembe yace yoparamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda cirema, ya m'gulu lace, monga umayesa mtengo wace pochula masekeli a siliva, kunena sekeli wa malo opatulika, ikhale nsembe yoparamula;