Leviticus 5:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono munthuyo abweze zopatulika zimene sadaperekezo, ndipo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse, ndipo azipereka kwa wansembe. Apo wansembeyo adzachita mwambo wopepesera machimo a munthuyo, popereka nsembe yopepesera kupalamula ya nkhosa yamphongo ija, ndipo munthuyo adzakhululukidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo abwezere cholakwira chopatulikacho, naonjezepo limodzi la magawo asanu, napereke kwa wansembe; ndi wansembeyo amchitire chomtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopalamula; ndipo adzakhululukidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo ayenera kubweza zinthu zopatulika zimene sanaperekezo. Awonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse ndi kuzipereka zonsezo kwa wansembe amene adzachita mwambo wopepesera machimo a munthuyo, popereka nkhosa yayimuna ija ngati nsembe yopepesera ndipo wochimwayo adzakhululukidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo abwezere colakwira copatulikaco, naonjezepo limodzi la magawo asanu, napereke kwa wansembe; ndi wansembeyo amcitire comtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yoparamula; ndipo adzakhululukidwa.