Leviticus 5:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abwere kwa wansembe ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema, imene mtengo wake ulingane ndi wa nyama ya nsembe yopepesera kupalamula. Wansembeyo achite mwambo wopepesera machimo amene munthuyo adachita mosadziŵawo, ndipo wochimwayo adzakhululukidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nadze nayo kwa wansembe nkhosa yamphongo yopanda chilema ya m'khola lake, monga umayesa mtengo wake, ikhale nsembe yopalamula; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera chifukwa cha kusachimwa dala kwake, osakudziwa; ndipo adzakhululukidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abwere kwa wansembe ndi chopereka chopepesera kupalamula kwake. Chopereka chikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake ukhale woyenera nsembe yopepesera kupalamula kumene anachimwa mosadziwako, ndipo munthuyo adzakhululukidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nadze nayo kwa wansembe nkhosa yamphongo yopanda cirema ya m'khola lace, monga umayesa mtengo wace, ikhale nsembe yoparamula; ndipo wansembeyo amcitire comtetezera cifukwa ca kusacimwa dala kwace, osakudziwa; ndipo adzakhululukidwa.