Leviticus 5:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu akakhudza chinthu chilichonse chonyansa pa zachipembedzo, monga nyama yakufa yam'thengo kapena yoŵeta, kapenanso zokwaŵa zakufa, ndipo pokhudzapo adziipitsa mosadziŵa, munthu ameneyo ndi woipitsidwa, ndiponso ndi wopalamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapena munthu akakhudza chilichonse chodetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa choweta chodetsa, kapena mtembo wa chokwawa chodetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi wopalamula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Munthu akakhudza chinthu chilichonse chodetsedwa, monga nyama yakufa ya mʼthengo, kapena chiweto chakufa kapenanso chokwawa chakufa, ngakhale iyeyo wachikhudza mosadziwa, wasanduka wodetsedwa ndipo wachimwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kapena munthu akakhudza ciri conse codetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa coweta codetsa, kapena mtembo wa cokwawa codetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi woparamula.