Leviticus 5:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina aliyense akakhudza zonyansa za munthu za mtundu uliwonse, ndipo pokhudzapo adziipitsa mosadziŵa, munthu ameneyo akhala wopalamula, akangozindikira pambuyo pake zimene wachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena akakhudza chodetsa cha munthu, ndicho chodetsa chilichonse akhala wodetsedwa nacho, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Munthu akakhudza choyipitsa munthu cha mtundu uliwonse, ndipo pochikhudzapo ndi kuyipitsidwa nacho mosadziwa, munthuyo adzakhala wopalamula akangodziwa chimene wachitacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena akakhudza codetsa ca munthu, ndico codetsa ciri conse akakhala codetsedwa naco, ndipo cidambisikira; koma pocizindikira akhala woparamula: