Leviticus 5:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu akalakwa polumbira mofulumira kuti adzachita chinthu choipa kapena chabwino, kulumbira kwake kwa mtundu uliwonse kumene anthu amachita, ndipo polumbirapo sadziŵa vuto lake, munthu ameneyo akhala wopalamula, akangozindikira pambuyo pake zimene wachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapena munthu akalumbira ndi milomo yake osalingirira kuchita choipa, kapena kuchita chabwino, chilichonse munthu akalumbira osalingirira, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula chimodzi cha izi:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Munthu akalumbira mofulumira kapena mosasamala kuti adzachita chinthu, choyipa kapena chabwino, ngakhale kuti wachita izi mosadziwa kuti nʼkulakwa, pamene wazindira kulakwa kwake, iye adzakhalabe wopalamula akangodziwa chimene wachitacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kapena munthu akalumbira ndi milomo yace osalingirira kucita coipa, kapena kucita cabwino, ciri conse munthu akalumbira osalingirira, ndipo cidambisikira; koma pocizindikira akhala woparamula cimodzi ca izi: