Leviticus 5:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka abwere kudzapereka nsembe kwa Chauta, chifukwa cha tchimo lakelo. Nsembe yake ikhale ya nkhosa yaikazi kapena ya mbuzi yaikazi. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera machimo a wopalamula uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nadze nayo nsembe yopalamula kwa Yehova chifukwa cha kulakwa kwake adachimwira, ndiyo nkhosa yaikazi, kapena mbuzi yaikazi, ikhale nsembe yauchimo; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake, munthuyo abwere kwa Yehova ndi mwana wankhosa wamkazi kapena mbuzi kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo ndipo wansembe achite mwambo wopepesera tchimo lomwe wachitalo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nadze nayo nsembe yoparamula kwa Yehova cifukwa ca kulakwa kwace adacimwira, ndiyo msoti wa nkhosa, kapena msoti wa mbuzi, ukhale nsembe yaucimo; ndipo wansembe amcitire comtetezera cifukwa ca kucimwa kwace.