Leviticus 5:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma ngati munthu alibe nkhosa kapena mbuzi, atenge njiŵa ziŵiri kapena nkhunda ziŵiri, kuti zikhale nsembe yopereka kwa Chauta yopepesera machimo ake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthuyo alibe mwana wankhosa, abweretse njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri kwa Yehova ngati chopereka chopepesera tchimo lake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera tchimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cuma cace cikapanda kufikira nkhosa, wocimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yace yoparamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yaucimo, ndi yina ya nsembe yopsereza.