Leviticus 5:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo awazeko magazi a mbalameyo m'mbali mwa guwa. Koma magazi ena otsala aŵathire pansi, kuti ayenderere patsinde pa guwalo. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nawazeko mwazi wa nsembe yauchimo pa mbali ya guwa la nsembe; ndi mwazi wotsalira aukamulire patsinde pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yauchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kenaka awaze magazi a chopereka chopepesera tchimocho mʼmbali mwa guwa. Magazi ena onse awathire pa tsinde la guwa. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nawazeko mwazi wa nsembe yaucimo pa mbali ya guwa la nsembe; ndi mwazi wotsalira aukamulire patsinde pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yaucimo.