Leviticus 6:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wansembe avale mkanjo wake wabafuta, avalenso kabudula wabafuta, ndipo atengeko phulusa la nyama yopsereza pa guwa ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto pa guwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono wansembe avale mkanjo wake wa nsalu yofewa ndi yosalala. Mʼkati avalenso kabudula wofewa, wosalala. Pambuyo pake atenge phulusa la nyama imene yatenthedwa pa guwa lansembe paja ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe abvale mwinjiro wace wabafuta, nabvale pathupi pace zobvala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, mota utanyeketsa nsembe yamoto pa guwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.