Leviticus 6:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Moto wapaguwa uzikhala uli chiyakire, usazime. Wansembe azisonkhezera motowo ndi nkhuni m'maŵa mulimonse, ndipo aziyala nsembe yopsereza paguwapo, ndi kupserezapo mafuta a nsembe zachiyanjano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo moto wa pa guwa la nsembe uyakebe pamenepo, wosazima; wansembe ayatsepo nkhuni m'mawa ndi m'mawa; nakonzepo nsembe yopsereza, natenthepo mafuta a nsembe zoyamika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Moto wa pa guwa uzikhala ukuyaka nthawi zonse, usamazime. Mmawa uliwonse wansembe aziwonjezerapo nkhuni pa motopo ndi kukonza nsembe yopsereza, ndi kutentha mafuta a nsembe yachiyanjano pamenepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mota wa pa guwa la nsembe uyakebe pamenepo, wosazima; wansembe ayatsepo nkhuni m'mawa ndi m'mawa; nakonzepo nsembe yopsereza, natenthepo mafuta a nsembe zoyamika.