Leviticus 6:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mmodzi atapeko dzanja limodzi la ufa wosalala woperekedwa ku nsembeyo, pamodzi ndi mafuta ndi lubani yense amene ali pa chopereka cha chakudyacho. Azitenthe pa guwa, kuti zikhale chikumbutso, ndipo zitulutse fungo lokomera Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa chopereka cha ufa wosalala, ndi pa mafuta ake, ndi lubani lonse lili pa chopereka chaufa, nazitenthe pa guwa la nsembe, zichite fungo lokoma, ndizo chikumbutso chake cha kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe mmodzi atapeko dzanja limodzi la ufa wosalala wa nsembe yachakudya ija kuti ukhala ufa wachikumbutso ndi mafuta pamodzi ndi lubani yense amene ali pa nsembe ya chakudyacho, ndipo azitenthe pa guwa kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse kuti zikhale nsembe ya fungo lokomera Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa copereka ca ufa wosalala, ndi pa mafuta ace, ndi libona lonse liri pa copereka caufa, nazitenthe pa guwa la nsembe, zicite pfungo lokoma, ndizo cikumbutso cace ca kwa Yehova.