Leviticus 6:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aroni ndi ana ake adye zimene zatsalapo. Zikhale zosafufumitsa, ndipo azidyere pa malo oyera, ndiye kuti pa bwalo la chihema chamsonkhano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chotsalira chake adye Aroni ndi ana ake; achidye chopanda chotupitsa m'malo opatulika; pa bwalo la chihema chokomanako achidye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aaroni ndi ana ake azidya zimene zatsala koma azidya zopanda yisiti ku malo wopatulika, ku bwalo la tenti ya msonkhano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cotsalira cace adye Aroni ndi ana ace; acidye copanda cotupitsa m'malo opatulika; pa bwalo la cihema cokomanako acidye.