Leviticus 6:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Poziphika asathiremo chofufumitsira. Ndaŵapatsa zotsalazo kuti zikhale gawo lao la nsembe zanga zopsereza. Zonsezo nzoyera kwambiri monga nsembe yopepesera machimo, ndiponso nsembe yopepesera kupalamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Asachiphike ndi chotupitsa. Ndachipereka chikhale gawo lao lochokera pa nsembe zanga zamoto; ndicho chopatulika kwambiri, monga nsembe yauchimo, ndi monga nsembe yopalamula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Poziphika asathire yisiti. Ndawapatsa zotsalazo kuti zikhale gawo lawo la nsembe zanga zopsereza. Zonsezi ndi zopatulika kwambiri monga nsembe yopepesera tchimo ndiponso nsembe yopepesera machimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Asaciphike ndi cotupitsa, Ndacipereka cikhale gawo lao locokera pa nsembe zanga zamoto; ndico copatulikitsa, monga nsembe yaucimo, ndi monga nsembe yoparamula.