Leviticus 6:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana onse aamuna a Aroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Chauta, monga kudalembedwa kuti zidzatero nthaŵi zonse pa mibadwo yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudze guwalo chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, chiwachokere ku nsembe zamoto za Yehova; aliyense wakuzikhudza izi adzakhala wopatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana aliyense wamwamuna wa Aaroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova. Ndi gawo lake lokhazikika la chopereka chopsereza kwa Yehova pa mibado yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudza nsembezo chidzakhala chopatulika.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, ciwacokere ku nsembe zamoto za Yehova; ali yense wakuzikhudza izi adzakhala wapatolika.