Leviticus 6:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwira Chauta chifukwa cha kunyenga mnzake pomakana kumubwezera mnzakeyo zimene adamsungiza, kapena kumubera, kapena kumnyenga,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akachimwa munthu nakachita mosakhulupirika pa Yehova nakachita monyenga ndi mnansi wake kunena za choikiza, kapena chikole, kapena chifwamba, kapena anasautsa mnansi wake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akacimwa munthu nakacita mosakhulupirika pa Yehova nakacita monyenga ndi mnansi wace kunenaza coikiza, kapena cikole, kapena cifwamba, kapena anasautsa mnansi wace;