Leviticus 6:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ipangidwe ndi mafuta pa chiwaya. Ubwere nacho ili yosakaniza bwino, yophikidwa mitandamitanda monga amachitira ndi chopereka cha chakudya. Ndipo aipereke kuti itulutse fungo lokomera Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chikonzeke pachiwaya ndi mafuta; udze nacho chokazinga; chopereka chaufa chazidutsu ubwere nacho, chikhale fungo lokoma la kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ipangidwe ndi mafuta pa chiwaya ndipo ubwere nayo ili yosakaniza bwino, yophikidwa mitandamitanda monga amachitira ndi nsembe yachakudya. Iphikidwe moti itulutse fungo lokomera Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cikonzeke paciwaya ndi mafuta; udze naco cokazinga; copereka caufa cazidutsu ubwere naco, cikhale pfungo lokoma la kwa Yehova.