Leviticus 6:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wansembe wa fuko la Aroni amene wadzozedwa kuti aloŵe m'malo mwake, aipereke kwa Chauta nthaŵi zonse monga kudalembedwera. Aipsereze nsembe yonse poti lamulo ndi lamuyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe wodzozedwa m'malo mwake, wa mwa ana ake, achite ichi; likhale lemba losatha; achitenthe konse kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wa fuko la Aaroni amene adzadzozedwe kukhala wansembe kulowa mʼmalo mwa Aaroni ndiye amene azidzakonza ndi kupereka nsembeyi kwa Yehova nthawi zonse monga kunalembedwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe wodzozedwa m'malo mwace, wa mwa ana ace, acite ici; likhale lemba losatha; acitenthe konse kwa Yehova.