Leviticus 6:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopepesera machimo ndi ili: pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza, aphereponso nsembe yopepesera machimo kwa Chauta. Imeneyo ndi nsembe yoyera kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lankhula ndi Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yauchimo ndi ichi: Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo pophera nsembe yauchimo pamaso pa Yehova; ndiyo yopatulika kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uza Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Malamulo a nsembe ya tchimo ndi awa: Nsembeyi iziphedwa pamaso pa Yehova pa malo pamene mumaphera nsembe yopsereza popeza ndi nsembe yopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lankhula ndi Aroni ndi ana ace, ndi kuti, Cilamulo ca nsembe yaucimo ndi ici: Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo pophera nsembe yaucimo pamaso pa Yehova; ndiyo yopatulikitsa.