Leviticus 6:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
munthu akachimwa pa zimenezi ndi wopalamula ndithu, abweze zimene adalandazo, zimene adatenga monyengazo, zomsungizazo, ndi zotayika zimene adatolazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo padzali kuti popeza anachimwa, napalamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwachifwamba, kapena chinthuchi adachiona ndi kusautsa mnzake, kapena choikiza anamuikiza, kapena chinthu chotayika anachipeza;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kubweza zimene anabazo, zimene analanda mwachinyengozo, zimene anamusungitsazo, zimene anatolazo
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo padzali kuti popeza anacimwa, naparamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwacifwamba, kapena cinthuci adaciona ndi kusautsa mnzace, kapena coikiza anamuikiza, kapena cinthu cotayika anacipeza;