Leviticus 6:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, abweze zonsezo ndi kuwonjezapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse, tsono amubwezere mwini wakeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapena chilichonse analumbirapo monama; achibwezere chonsechi, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ichi kwa mwini wake tsiku lotsutsidwa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kapena ciri conse analumbirapo monama; acibwezere conseci, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ici kwa mwini wace tsiku lotsutsidwa iye.