Leviticus 7:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
akaipereka chifukwa cha kuthokoza, pamodzi ndi nsembe yothokozerayo apereke makeke osafufumitsa, osakaniza ndi mafuta, timitanda ta buledi wosafufumitsa, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wosakaniza bwino ndi mafuta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthuyo apereka chifukwa cha kuthokoza, apereke nsembeyo pamodzi ndi makeke wopanda yisiti, osakaniza ndi mafuta; timitanda ta buledi wopanda yisiti, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wophikidwa bwino, wosakaniza ndi mafuta.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndinsembe yolemekeza, timitanda topanda cotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda cotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tooca, ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta.