Leviticus 7:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyama ya nsembe yachiyanjano yothokozerayo aidye pa tsiku lopereka nsembe yakeyo. Asaisungeko mpang'ono pomwe kufikira m'maŵa mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunena za nyama ya nsembe yolemekeza ya nsembe zoyamika zake, aziidya tsiku lomwelo lakuipereka; asasiyeko kufikira m'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyama ya nsembe yachiyanjano yothokozera idyedwe pa tsiku lomwe nsembeyo yaperekedwa ndipo isatsaleko mpaka mmawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunena za nyama ya nsembe volemekeza ya nsembe zoyamika zace, aziidya tsiku lomwelo lakuipereka; asasiyeko kufikira m'mawa.