Leviticus 7:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma nsembe yake ikakhala yoti waipereka moilumbirira kapena mwaufulu, aidye pa tsiku lomwe akuiperekalo, ndipo nyama yotsala aidye m'maŵa mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma nsembe ya chopereka chake ikakhala ya chowinda, kapena chopereka chaufulu, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yake; ndipo m'mawa adye chotsalirapo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma ngati nsembe yakeyo apereka chifukwa cha lumbiro kapena mwaufulu, nsembeyo adye tsiku lomwe yaperekedwalo. Koma yotsala angathe kuyidya mmawa mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma nsembe ya copereka cace ikakhala ya cowinda, kapena copereka caufuhi, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yace; ndipo m'mawa adye cotsalirapo;