Leviticus 7:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo wina aliyense akakhudza chinthu chonyansa pa zachipembedzo, kaya nchonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, tsono nadyako nyama ya nsembe yachiyanjano yopereka kwa Chauta, munthuyo achotsedwe pakati pa Aisraele anzake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu akakhudza chinthu chodetsa, chodetsa cha munthu, kapena chodetsa cha zoweta, kapena chilichonse chonyansa chodetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati munthu wina akhudza chinthu chodetsedwa, kaya chonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, ndipo kenaka nʼkudya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, munthu ameneyo achotsedwe pakati anthu a mtundu wake.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu akakhudza cinthu codetsa, codetsa ca munthu, kapena codetsa ca zoweta, kapena ciri conse conyansa codetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.