Leviticus 7:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafuta a nyama yofa yokha, ndi mafuta a nyama yojiwa ndi zilombo, angathe kuŵagwiritsa ntchito zina zilizonse, koma iwowo asadye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi chilombo ayenera ntchito iliyonse, koma musamadya awa konsekonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafuta a nyama yofa yokha, kapena mafuta a nyama yophedwa ndi zirombo akhoza kuwagwiritsa ntchito iliyonse, koma inu musadye mafuta amenewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi cirombo ayenera nchito iri yonse, koma musamadya awa konse konse.