Leviticus 7:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho nganga yopereka moweyula manjayo, pamodzi ndi ntchafu yoperekayo, ndikuzichotsa zonsezo kwa Aisraele. Ndikuzichotsa pa nsembe zao zachiyanjano, ndipo ndikuzipereka kwa wansembeyo Aroni ndi kwa ana ake, kuti zikhale chigawo chao nthaŵi zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndatengako kwa ana a Israele, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ake, zikhale zoyenera iwo kosatha zochokera kwa ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho pa zopereka zachiyanjano za Aisraeli, Ine ndatengapo chidale chomwe amaweyula ndi ntchafu zimene amapereka nsembe ndipo ndazipereka kwa wansembe Aaroni ndi ana ake. Izi ndizo gawo lawo nthawi zonse pa zopereka za Aisraeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndatengako kwa ana a Israyeli, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ace, zikhale zoyenera iwo kosatha zocokera kwa ana a Israyeli.