Leviticus 7:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta ndiye amene adalamula Aisraele kuti azipereka zimenezi kwa ansembe, pa tsiku limene adadzozedwa. Zimenezo ndizo chigawo chao nthaŵi zonse pa mibadwo yao yonse.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
limene Yehova anauza ana a Israele aziwapatsa, tsiku limene Iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova ndiye analamulira kuti pa zopereka za Aisraeli azitapapo zimenezi ndi kuwapatsa ansembe ngati gawo lawo. Yehovayo analamula zimenezi pa tsiku limene ansembewo anapatulidwa ndipo anachikhazikitsa ngati lamulo la nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
limene Yehova anauza ana a Israyeli aziwapatsa, tsiku limene iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.