Leviticus 7:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wamwamuna aliyense wa m'banja la ansembe angathe kudyako. Aidyere pa malo oyera. Imeneyo ndiyo nsembe yoyera kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulika kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kudyako nsembeyo koma adyere ku malo opatulika. Imeneyi ndi nsembe yopatulika kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulikitsa.