Leviticus 8:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adawazako mafuta ena kasanu ndi kaŵiri pa guwa, nalidzoza guwalo pamodzi ndi zipangizo zake zonse. Adadzozanso mkhate pamodzi ndi phaka lake, kuti zikhale zopatulika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake, kuzipatula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawaza mafuta ena pa guwa kasanu ndi kawiri, nalidzoza guwalo pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso beseni ndi tsinde lake, nazipatula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate ndi tsinde lace, kuzipatula.