Leviticus 8:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Mose adabwera ndi ng'ombe yamphongo ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aroni ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pa mutu wa ng'ombe ya nsembe yauchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mose anabwera ndi ngʼombe yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aaroni ndi ana ake anasanjika manja awo pamutu pa ngʼombeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yaucimo; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pa mutu wa ng'ombe ya nsembe yaucimo.