Leviticus 8:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Mose adaipha natenga magazi ake ndi kuŵapaka ndi chala chake pa nyanga za guwa molizungulira, ndipo adaliyeretsa. Adathiranso magazi patsinde pa guwalo nalipatula. Motero adachita mwambo wopepesera machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi chala chake pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde pa guwa la nsembe, nalipatula, kuti alichitire cholitetezera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anapha ngʼombeyo, ndi kutenga magazi ena angʼombeyo ndi kupaka ndi chala chake pa nyanga zaguwa lansembe, naliyeretsa. Magazi otsalawo anawakhuthulira pa tsinde laguwalo. Motero anachita mwambo wopepesera machimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi cala cace pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde pa guwa la nsembe, nalipatula, kuti alicitire colitetezera.