Leviticus 8:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atatsuka matumbo ake ndi miyendo yake, adazitenthanso. Motero adatentha nkhosa yathunthuyo pa guwa, kuti ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma, yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta, monga momwe Iye adaalamulira Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anatsuka matumbo ake ndi miyendo yake, ndi kutentha nkhosa yonseyo pa guwa lansembe kuti ikhale nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yachakudya yoperekedwa kwa Yehova monga Yehovayo analamulira Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yocita pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.