Leviticus 8:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mose adapereka nkhosa ina yamphongo, yoyenerera pa mwambo wodzoza ansembe. Ndipo Aroni pamodzi ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pa mutu wa mphongoyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mose anapereka nkhosa yayimuna ina pamwambo wodzoza ansembe, ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna anasanjika manja awo pamutu pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pa mutu wa mphongoyo.