Leviticus 8:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adabwera ndi ana a Aroni, ndipo Mose adapaka magazi pa nsonga za makutu ao a ku dzanja lamanja ndi pa zala zao zazikulu za ku dzanja lamanja, ndiponso pa zala zao zazikulu za ku phazi la ku dzanja lamanja. Kenaka Mose adathira magazi pa guwa molizungulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anabwera nao ana amuna a Aroni, ndi Mose anatengako mwazi, naupaka pa ndewerere ya khutu lao la ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lao, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao la ku dzanja lamanja; ndipo Mose anawaza mwaziwo pa guwa la nsembe pozungulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Mose anabwera ndi ana aamuna a Aaroni ndi kupaka magazi pa ndewere za makutu awo akumanja, pa zala zawo zazikulu za dzanja lamanja, ndiponso pa zala zawo zazikulu za kuphazi lakumanja. Kenaka iye anawaza magazi otsalawo mbali zonse za guwalo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anabwera nao ana amuna a Aroni, ndi Mose anatengako mwazi, naupaka pa ndewerere ya khutu lao la ku dzanja lamanja, ndi pa cala cacikuru ca ku dzanja lamanja lao, ndi pacala cacikuru ca phazi lao la ku dzanja lamanja; ndipo Mose anawaza mwaziwo pa guwa la nsembe pozungulira,