Leviticus 8:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatenga mafuta, mchira wamafuta, mafuta onse akumatumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, imso ziŵiri ndi mafuta ake omwe, ndi ntchafu ya ku dzanja lamanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatenga mafutawo ndi mchira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anatenganso mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake ndiponso ntchafu yakumanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatenga mafutawo ndi mcira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi cokuta ca mphafa, ndi imso ziwiri, ndi mafuta ace, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;