Leviticus 8:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo m'dengu la buledi wosafufumitsa, lopatulikira Chauta, adatengamo mtanda umodzi wa buledi wosafufumitsa, mtanda umodzi adatengamo mtanda umodzi wa buledi wosafufumitsa, mtanda umodzi wopaka mafuta ndi mtanda umodzi wa buledi wopyapyala. Zonsezo ataziika pa mafuta aja ndi pa ntchafu ya ku dzanja lamanja ija,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mʼdengu la buledi wopanda yisiti limene linali pamaso pa Yehova, anatengamo buledi mmodzi, buledi mmodzi wokhala ndi mafuta a olivi, ndi buledi wopyapyala mmodzi. Zonsezi anaziyika pa mafuta aja ndi pa ntchafu ya ku dzanja lamanja ija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mu mtanga wa mkate wopanda cotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda cotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;