Leviticus 8:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adauza Aroni ndi ana ake kuti, “Muphike nyamayo pa khomo la chihema chamsonkhano, ndipo muidyere pomwepo, pamodzi ndi buledi amene ali m'dengu la zopereka pa mwambo wodzoza ansembe, potsata zimene Chauta adaalamula kuti, ‘Aroni pamodzi ndi ake ndiwo adzadye zimenezo.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ake amuna, Phikani nyamayi pakhomo pa chihema chokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu dengu la nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ake aidye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anawuza Aaroni ndi ana ake kuti, “Phikani nyamayo pa khomo la tenti ya msonkhano, ndipo mudyere pomwepo pamodzi ndi buledi amene ali mʼdengu la zopereka za pamwambo wodzoza ansembe monga Yehova analamulira kuti, ‘Aaroni ndi ana ake azidya zimenezi.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ace amuna, Phikani nyamayi pakhomo pa cihema cokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu mtanga wa nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ace aidye.