Leviticus 8:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo pa masiku asanu ndi aŵiri musatulukire kunja kwa chihema chamsonkhano, mpaka masiku a mwambo wodzoza ansembe atatha, poti mwambowu ndi wa masiku asanu ndi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo musatuluka pa khomo la chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, kufikira anakwanira masiku a kudzaza manja kwanu; pakuti adzaze manja anu masiku asanu ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musatuluke kunja kwa tenti ya msonkhano kwa masiku asanu ndi awiri mpaka masiku amwambo wokudzozani unsembe atatha, pakuti mwambowu ndi wa masiku asanu ndi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo musaturuka pa khomo la cihema cokomanako masiku asanu ndi awiri, kufikira anakwanira masiku a kudzaza manja kwanu; pakuti adzaze manja anu masiku asanu ndi awiri.