Leviticus 9:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adapereka zopereka za anthuwo, natenga mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthuwo, naipha nkuipereka ngati nsembe yopepesera machimo, monga adachitira ndi nsembe yopepesera machimo yoyambayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwera nacho chopereka cha anthu, natenga mbuzi ya nsembe yauchimo ndiyo ya kwa anthu, naipha, naipereka nsembe yauchimo, monga yoyamba ija.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Aaroni anapereka zopereka za anthuwo. Anatenga mbuzi yopepesera machimo a anthuwo, yopereka chifukwa cha tchimo, nayipha ndi kuyipereka kuti ikhale yopepesera machimo monga anachitira ndi nsembe yoyamba ija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabwera naco copereka ca anthu, natenga mbuzi ya nsembe yaucimo ndiyo ya kwa anthu, naipha, naipereka nsembe yaucimo, monga yoyamba ija.