Leviticus 9:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adaphanso ng'ombe ndi nkhosa yamphongo, kuperekera anthu nsembe yachiyanjano. Pambuyo pake ana a Aroni adampatsira magazi, ndipo iye adathira magaziwo pa guwa molizungulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anaphanso ng'ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozungulira,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Aaroni anapha ngʼombe ndi nkhosa yayimuna monga nsembe yachiyanjano ya anthu. Ana ake anamupatsira magazi ndipo anawawaza mbali zonse za guwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anaphanso ng'ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozungulira, ndi mafuta a ng'ombe;