Leviticus 9:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adauza Aroniyo kuti, “Utenge mwanawang'ombe wamphongo kuti akhale nsembe yopepesera machimo, ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza. Zonsezo zikhale zopanda chilema, ndipo uzipereke pamaso pa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anati kwa Aroni, Dzitengere mwanawang'ombe wamwamuna, akhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopsereza, zopanda chilema, nubwere nazo pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anawuza Aaroni kuti, “Tenga mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yako yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza. Zonsezi zikhale zopanda chilema ndipo uzipereke pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anati kwa Aroni, Dzitengere mwana wa ng'ombe wamwamuna, akhale nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopsereza, zopanda cirema, nubwere nazo pamaso pa Yehova.