Leviticus 9:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pompo moto udatuluka pamaso pa Chauta nupserezeratu nsembe yopsereza ndi mafuta omwe, zimene zinali paguwapo. Ndipo anthu ataona motowo, adafuula naŵeramitsa nkhope zao pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo unatuluka moto pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta pa guwa la nsembe; ndipo pakuchiona anthu onse anafuula, nagwa nkhope zao pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pomwepo moto unatuluka pamaso pa Yehova niwutentha nsembe zopsereza ndi mafuta zimene zinali pa guwa. Anthu onse ataona zimenezi anafuwula mwachimwemwe ndipo anaweramitsa nkhope zawo pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo unaturuka mota pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta pa guwa la nsembe; ndipo pakuciona anthu onse anapfuula, nagwa nkhope zao pansi.