Leviticus 9:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono uuze Aisraele kuti, ‘Tengani tonde kuti muperekere nsembe yopepesera machimo. Mutengenso mwanawang'ombe ndi mwanawankhosa. Aŵiri onsewo akhale a chaka chimodzi, opanda chilema, kuti akhale nsembe yopsereza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nunene kwa ana a Israele, ndi kuti, Dzitengereni tonde akhale nsembe yauchimo; ndi mwanawang'ombe, ndi mwanawankhosa, a chaka chimodzi, opanda chilema, akhale nsembe yopsereza;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka uwawuze Aisraeli kuti, ‘Tengani mbuzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Mutengenso mwana wangʼombe ndi mwana wankhosa. Zonsezi zikhale za chaka chimodzi ndi zopanda chilema kuti zikhale nsembe yopsereza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nunene kwa ana a Israyeli, ndi kuti, Dzitengereni tonde akhale nsembe yaucimo; ndi mwana wa ng'ombe, ndi mwana wa nkhosa, a caka cimodzi, opanda cirema, akhale nsembe yopsereza;