Leviticus 9:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mutengenso ng'ombe ndi nkhosa kuti zikhale nsembe zachiyanjano zoti aziphere pamaso pa Chauta. Mubwerenso ndi zopereka za zakudya zosakaniza ndi mafuta, pakuti lero Chauta akuwonekerani.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo zikhale zakuyamika, kuziphera nsembe pamaso pa Yehova; ndi nsembe yaufa yosanganiza ndi mafuta; pakuti lero Yehova wakuonekerani inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mutengenso ngʼombe yayimuna ndi nkhosa yayimuna kuti zikhale nsembe yachiyanjano zoti ziperekedwe pamaso pa Yehova. Pamodzi ndi izi mubwerenso ndi nsembe yachakudya yosakaniza ndi mafuta pakuti lero Yehova akuonekerani.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo zikhale zakuyamika, kuziphera nsembe pamaso pa Yehova; ndi nsembe yaufa yosanganiza ndi mafuta; pakuti lero Yehova wakuonekerani inu.