Leviticus 9:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Moseyo adauza Aroni kuti, “Sendera pafupi ndi guwa, ndipo upereke nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, kuti uchite mwambo wopepesera machimo ako ndi machimo a Aisraele. Ubwere ndi zopereka za anthuwo ndipo uchite mwambo wopepesera machimo ao, monga momwe Chauta walamulira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Sendera kufupi kwa guwa la nsembe, nukonze nsembe yako yauchimo, ndi nsembe yako yopsereza, nudzichitire wekha ndi anthuwo chotetezera; nupereke chopereka cha anthu, ndi kuwachitira chotetezera; monga Yehova anauza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Mose anawuza Aaroni kuti, “Sendera pafupi ndi guwa ndipo upereka nsembe yako yopepesera machimo ndi nsembe yako yopsereza ndikuchita mwambo wopepesera machimo ako ndi machimo a anthu. Anthuwa apereke nsembe zawo zopepesera machimo monga momwe Yehova walamulira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Sendera kufupi kwa guwa la nsembe, nukonze nsembe yako yaucimo, ndi nsembe yako yopsereza, nudzicitire wekha ndi anthuwo cotetetezera; nupereke coperekaca anthu, ndi kuwacitira cotetezera; monga Yehova anauza.