Luke 1:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mngeloyo adamuuza kuti, “Usaope, Zakariya, Mulungu wamva pemphero lako. Mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mngeloyo anati kwa iye: “Usachite mantha, Zakariya; pemphero lako lamveka. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wamwamuna ndipo udzamutche dzina loti Yohane.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zakariya, cifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yohane.