Luke 1:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
popeza kuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Sazidzamwa konse vinyo kapena choledzeretsa china chilichonse. Adzakhala wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ngakhale asanabadwe nkomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Iye sadzamwa vinyo kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo adzazadzidwa ndi Mzimu Woyera kuyambira pa kubadwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti iye adzakhala wamkuru pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena, kacasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.