Luke 1:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Molimba mtima ndiponso mwamphamvu monga mneneri Eliya, adzatsogolako Ambuye akubwera. Adzayanjanitsanso makolo ndi ana ao, adzatembenuza anthu osamvera kuti akhale ndi nzeru zonga za anthu olungama. Adzakonzera Ambuye anthu okonzekeratu kuŵatumikira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iye adzabwera Ambuye asanabwere mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya. Adzatembenuzira mitima ya abambo kwa ana awo ndi osamvera ku nzeru ya olungama, kuthandiza anthu kuti akonzekere kubwera kwa Ambuye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzamtsogolera iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.