Luke 1:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zakariya adafunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingadziŵe bwanji kuti zimenezi nzoona? Ineyo ndine nkhalamba, mkazi wanga nayenso wakalamba.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Zekariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ichi ndi chiyani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zake za mkazi wanga zachuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zakariya anamufunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Ine ndine wokalamba ndipo mkazi wanga ali ndi zaka zambiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Zakariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ici ndi ciani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zace za mkazi wanga zacuruka.